Luke 16:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘Nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anamuyitana ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi nʼchiyani chimene ndikumva za iwe? Pereka tsatanetsatane wa ntchito yako, pakuti supitirizanso kukhala kapitawo wanga.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuitana, nati kwa iye, ici ndi ciani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao.