Luke 16:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Abrahamu adati, ‘Mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zoŵaŵa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukila kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.