Luke 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘Ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima, ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso, kukundichititsa manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kapitawoyo analingalira kuti, ‘Kodi tsopano ndidzachita chiyani? Bwana wanga andichotsa ntchito. Ine ndilibe mphamvu zokwanira zolimira, komanso ine ndimachita manyazi kupempha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwace, Ndidzacita ciani, cifukwa mbuye wanga andicotsera ukapitao? kulima ndiribe mphamvu, kupemphapempha kundicititsa manyazi.