Luke 16:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adaitana angongole a mbuye wake mmodzimmodzi. Adafunsa woyamba kuti, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa mbuye wanga?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wake, nanena kwa woyamba, Unakongola chiyani kwa mbuye wanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho iye anayitana aliyense amene anali ndi ngongole kwa bwana wake. Iye anafunsa woyamba, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa bwana wanga?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wace, nanena kwa woyamba, Unakongola ciani kwa mbuye wanga?