Luke 16:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adati, ‘Mafuta amuyeso wokwanira mitsuko makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako yangongole, khala pansi msanga, ungolembapo mitsuko makumi asanu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata wako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’ “Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata wako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.