Luke 16:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mbuye wa kapitao wonyenga uja adamuyamikira chifukwa cha kuchenjera kwake. Pajatu pokhala ndi anzao, anthu ongokonda zapansipano ngochenjera koposa anthu okhala m'kuŵala kwa Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mbuye wace anatama kapitao wonyengayo, kuti anacita mwanzeru; cifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.