Luke 16:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu popitiriza mau adati, “Ndipo Ine ndikukuuzani kuti mudzipezere abwenzi ndi chuma chonyengachi. Apo chumacho chikadzakutherani, Mulungu adzakulandirani ku nyumba zamuyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikukuwuzani inu, gwiritsani ntchito chuma cha dziko lapansi kuti mudzipezere nokha abwenzi, kuti pamene chatha mudzalandiridwe mʼmalo okhala amuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi cuma cosalungama; kuti pamene cikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha.