Luke 17:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nichiwaononga onsewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'cingalawa, ndipo cinadza cigumula, niciwaononga onsewo.