Luke 17:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anayankha kuti, “Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ambuye anati, Mukakhala naco cikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.