Luke 18:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfarisiyo adaimirira nayamba kupemphera motere mumtima mwake: ‘Mulungu, ndikukuyamikani kuti ine sindili monga anthu ena onse ai. Iwowo ndi anthu akuba, osalungama ndi adama. Sindilinso monga wokhometsa msonkho uyu ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, acigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;