Luke 18:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwace woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzacepetsedwa; koma wodzicepetsa yekha adzakulitsidwa.