Luke 18:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ophunzira aja sadamvetse konse zimenezi. Tanthauzo la mau ameneŵa linali lobisika kwa iwo, nchifukwa chake sadamvetsetse zimene Yesu ankanenazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sanadziwitsa kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikira zonenedwazo.