Luke 18:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene anali patsogolo adamzazira, adati, “Khala chete!” Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale chete; koma iye anafuulitsa chifuulire, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale cete; koma iye anapfuulitsa cipfuulire, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.