Luke 18:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yomweyo adapenyanso nayamba kutsata Yesu, akuthokoza Mulungu. Anthu onse aja ataona zimenezi, adatamanda Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anacitira Mulungu mayamiko.