Luke 19:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ankamva zimene Yesu ankalankhula. Tsono adaŵaphera fanizo, popeza kuti anali pafupi ndi Yerusalemu, ndipo anthuwo ankaganiza kuti Mulungu akhazikitsa ufumu wake posachedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakumva izi iwo, iye anaonjeza nanena fanizo, cifukwa anali iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.