Luke 19:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaitana khumi mwa antchito ake naŵapatsa ndalama zasiliva khumi, aliyense yakeyake. Adaŵauza kuti, ‘Bachita nazoni malonda mpaka nditabwera.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaitana akapolo ace khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi, nati kwa iwo, Cita nazoni malonda kufikira ndibweranso.