Luke 19:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbuye wake adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zochepa kwambiri, udzalamulira midzi khumi.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Cabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'cacing'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi.