Luke 19:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa, ndikutsutsa ndi mau ako omwe. Kani unkadziŵa kuti ndine munthu wankhwidzi, amene ndimalonjerera zimene sindidaikize, ndipo ndimakolola zimene sindidabzale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiika, ndi wotuta chimene sindinachifesa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula cimene sindinaciika, ndi wotuta cimene sindinacifesa;