Luke 19:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake pa phiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau akulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuyandikira iye tsono potsetsereka pace pa phiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau akuru, cifukwa ca nchito zonse zamphamvu anaziona;