Luke 19:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzakusakaziratu iweyo pamodzi ndi anthu ako onse. Sadzasiya mwa iwe mwala pamwamba pa unzake, chifukwa chakuti sudazindikire nthaŵi imene Mulungu adaati adzakupulumutse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake; popeza sunazindikira nyengo ya mayang'aniridwe ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzace; popeza sunazindikira nyengo, ya mayang'aniridwe ako.