Luke 2:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikuru, cimene cidzakhala kwa anthu onse;