Luke 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Angelowo atachoka kubwerera Kumwamba, abusa aja adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tipite ku Betelehemu, tikaone zachitikazi, zimene Ambuye atidziŵitsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali, pamene angelo anacokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzace, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone cinthu ici cidacitika, cimene Ambuye anatidziwitsira ife.