Luke 2:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Simeoniyo adaŵadalitsa, nauza Maria, mai wa mwanayo, kuti, “Mwanayu Mulungu wamuika kuti Aisraele ambiri adzagwe, ambirinso adzadzuke, chifukwa cha iyeyu. Adzakhala chizindikiro chochokera kwa Mulungu, chimene anthu ambiri adzatsutsana nacho,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: “Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Mariya amace, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa. Israyeli; ndipo akhale cizindikilo cakutsutsana naco;