Luke 2:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziŵiri zokha,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panalinso mneneri wamkazi, dzina lake Ana, mwana wa Fanuelo, wa fuko la Aseri. Anali wokalamba kwambiri; anakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri atakwatiwa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanueli, wa pfuko la Aseri; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wace, kuyambira pa unamwali wace,