Luke 2:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adafikako nthaŵi yomweyo, nayamba kuyamika Mulungu, nkumakamba za Mwanayo ndi anthu onse amene ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, nabvomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za iye kwa anthu onse 1 akuyembekeza ciombolo ca Yerusalemu.