Luke 2:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m'banja ndi fuko la Davideyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumudzi wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe yemwe anakwera kucokera ku Galileya, ku mudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, ku mudzi wa Davine, dzina lace Betelehemu, cifukwa iye anali wa banja ndi pfuko lace la Davine;