Luke 2:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma iwo anayesa kuti Iye ali m'chipiringu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna Iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma iwo anayesa kuti iye ali m'cipiringu ca ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao;