Luke 20:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma alimi aja atamuwona, adayamba kuuzana kuti, ‘Uyu ndiye amene adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzake, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzace, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti colowa cace cikhale cathu.