Luke 20:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adamuponya kunja kwa mundawo, namupha. Kodi mwini munda wamphesa uja adzaŵatani alimi aja?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha. Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawachitira chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha. “Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha, Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawacitira ciani?