Luke 20:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adaŵayang'ana nati, “Nanga tsono tanthauzo lake nchiyani Malembo aŵa akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iye anawapenyetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chinalembedwa, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unakhala mutu wa pangodya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti, “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana wasanduka mwala wa pa ngodya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye anawapenyetsa iwo, nati, Nciani ici cinalembedwa, Mwala umene anaukana omanga nyumba, Womwewu unakhala mutu wa pangondya.