Luke 20:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a ansembe adaadziŵa kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo. Nchifukwa chake ankafuna kumugwira nthaŵi yomweyo, koma ankaopa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aphunzitsi amalamulo ndi akulu a ansembe amafuna njira yoti amuphe nthawi yomweyo, chifukwa anadziwa kuti ananena fanizo ili powatsutsa iwo. Koma iwo anali ndi mantha chifukwa cha anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo alembi ndi ansembe akuru anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.