Luke 20:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ozondawo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumalankhula ndi kuphunzitsa molungama, simuyang'anira kuti uyu ndani. Mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamfunsa iye, nanena, Mphunzitisi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;