Luke 20:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aphunzitsi, Mose adatilembera lamulo lakuti, ‘Ngati munthu amwalira, nasiya mkazi wake, koma opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera ife, kuti mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo alibe mwana iye, mbale wake adzakwatira mkaziyo, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera ire, kuti mbale wace wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo ali be mwana iye, mbale wace adzakwatira mkaziyo, nadzamuukitsira mbale wace mbeu.