Luke 20:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma zakuti anthu adzauka kwa akufa, Mose yemwe adaanenapo kale. Paja pa mbiri ija ya chitsamba choyaka moto, iye akuŵatchula Ambuye kuti, ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Citsamba cija, pamene iye amchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.