Luke 20:46 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika. Amakonda mipando yaulemu kwambiri m'nyumba zamapemphero ndiponso malo olemekezeka pa maphwando.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda obvala miinjiro, nakonda kulankhulidwa m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamapwando;