Luke 20:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Yesu adaphera anthu aja fanizo lina. Adati, “Munthu wina adaalima munda wamphesa. Adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina, nakakhalako nthaŵi yaitali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wamphesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wamphesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka ku dziko lina, nagonerako nthawi yaikuru.