Luke 21:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo. Pakuti padzagwa masautso aakulu pa dziko lino, ndipo Mulungu adzaŵakwiyira Aisraeleŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! Pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zidzakhala zoopsa nthawi imenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! Kudzakhala masautso aakulu mʼdziko ndipo anthu onse adzawakwiyira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! pakuti padzakhala cisauko cacikuru padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.