Luke 21:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzaphedwa pa nkhondo yoopsa, nkutengedwa ngati akapolo a anthu a mitundu ina. Kenaka Yerusalemu akunja adzampondereza mpaka pa mapeto ake a nthaŵi ya akunjawo.” Dan. 9.26; Mika 3.12; Zak. 11.6.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndi kutengedwa ukapolo kupita ku mayiko wonse. Yerusalemu adzaponderezedwa ndi anthu a mitundu ina mpaka nthawi ya a mitundu ina itakwaniritsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.