Luke 21:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku onse Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, koma usiku ankatuluka kukakhala ku phiri lotchedwa Phiri la Olivi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa m'Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona pa phiri lotchedwa la Azitona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo usana uli wonse iye analikuphunzitsa m'Kacisi; ndi usiku uli wonse anaturuka, nagona pa phiri lochedwa la Azitona.