Luke 21:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwace anaikamo za moyo wace, zonse anali nazo.