Luke 21:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena ankalankhula za Nyumba ya Mulungu kuti adaikongoletsa ndi miyala yokoma, ndiponso ndi mitulo yopereka kwa Mulungu. Yesu adati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene ena analikunena za Kachisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati Iye,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene ena analikunena za Kacisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati iye,