Luke 22:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, ici ndi thupi langa lopatsidwa cifukwa ca inu; citani ici cikumbukilo canga.