Luke 22:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaŵauza kuti, “Pakati pa anthu akunja, mafumu amadyera anthu ao masuku pa mutu, ndipo amene amaŵaonetsa mphamvu zao, amatchedwa mfulu zopatsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, Ochitira zabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awacitira ufumu; ndipo iwo amene awacitira ulamuliro anenedwa, Ocitira zabwino.