Luke 22:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi wamkulu ndani? Ndi amene alikudya, kapena amene akumtumikira? Si amene alikudyayo nanga? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumukira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wamkulu ndani, iye wakuseama pachakudya kapena wakutumikirapo? Si ndiye wakuseama pachakudya kodi? Koma Ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wamkuru ndani, iye wakuseama pacakudya kapena wakutumikirapo? si ndiye wakuseama pacakudya kodi? koma Ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira.