Luke 22:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndikunenetsa kuti ziyenera kuchitikadi mwa Ine zimene Malembo adanena kuti, ‘Ankamuyesa mmodzi mwa anthu ophwanya malamulo.’ Ndipo zonse zimene zidalembedwa za Ine zikuchitikadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndinena ndi inu, cimene cidalembedwa ciyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine ziri naco cimariziro.