Luke 22:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yesu adatuluka mu mzinda napita ku Phiri la Olivi monga adaazoloŵera. Ndipo ophunzira ake adapita naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anaturuka, napita monga adafucita, ku phiri la Azitona ndi ophunzira anamtsata iye.