Luke 22:56 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtsikana wina wantchito adamuwona atakhala nao pamotopo. Adamuyang'anitsitsa, nati, “Aŵansotu anali naye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwake kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwace kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye.