Luke 22:60 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Petro adati, “Munthu iwe, sindikuzidziŵa zimene ukunenazi.” Ndipo pompo, akulankhulabe, tambala adalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chilankhulire, tambala analira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa cimene ucinena, Ndipo pomwepo, iye ali cilankhulire, tambala analira.