Luke 22:66 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kutacha, a m'Bungwe Lalikulu la Ayuda adasonkhana, ndiye kuti akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Adatenga Yesu napita naye ku Bwalo lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 13 pamene kunaca, bungwe la akuru a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe akuru ndi alembi; ndipo anapita naye ku bwalo lao, nanena, 14 Ngati uli Kristu, utiuze.