Luke 22:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku la buledi wosafufumitsa lidafika, ndiye kuti tsiku limene anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku la mikate yopanda cotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paskha.